1.TINGATHE KUKHULUPILIRA MULUNGU

Nthawi ina Jim anafunsa munthu wosakhulupirira ngati anayamba waganizapo mozama ngati kunjakuno kuli Mulungu kapena ai.
Mwatchutchutchu, munthuyu anati kwa Jim, "zaka za m'mbuyomu pamene mwana wathu woyamba anabadwa; ndinatsala pang'ono kukhulupirira kuti Mulungu aliko; poona kamunthu kakang'ono kangwiro mu kama wake; tidzala take tikugwedera ndi timaso take tikuphethira. Kwa miyezi ingapo ndinali pafupi kusintha maganizo anga akuti kumwamba kulibe Mulungu" Izi zinamudabwitsa Jim.
"Pokaona kamwanako, ndinatsala pang'ono kukwanitsidwa kuti kuyenera kukhala Mulungu". Anapitiriza motero.
VOP Chichewa lesson download file
